Hosea 9

Chilango cha Israeli

1Iwe Israeli, usakondwere;
monga imachitira mitundu ina.
Pakuti wakhala wosakhulupirika kwa Mulungu wako;
umakonda malipiro a chiwerewere
pa malo aliwonse opunthira tirigu.
2Malo opunthira tirigu ndi malo opsinyira mphesa sadzadyetsa anthu;
adzasowa vinyo watsopano.
3Sadzakhalanso mʼdziko la Yehova.
Efereimu adzabwerera ku Igupto
ndipo mudzadya chakudya chodetsedwa ku Asiriya.
4Iwo sadzaperekanso chopereka cha chakumwa kwa Yehova,
kapena nsembe zawo kuti akondweretse Yehovayo.
Nsembe zotere zidzakhala kwa iwo ngati chakudya cha anamfedwa;
onse akudya chakudya chimenechi adzakhala odetsedwa.
Chakudya ichi chidzakhala chodya okha,
sichidzalowa mʼnyumba ya Yehova.

5Kodi mudzachita chiyani pa tsiku la maphwando anu oyikika;
pa masiku a zikondwerero za Yehova?
6Ngakhale iwo atathawa chiwonongeko,
Igupto adzawasonkhanitsa,
ndipo Mefisi adzawayika mʼmanda.
Khwisa adzamera pa ziwiya zawo zasiliva,
ndipo minga idzamera mʼmatenti awo.
7Masiku achilango akubwera,
masiku obwezera ali pafupi.
Israeli adziwe zimenezi.
Chifukwa machimo anu ndi ochuluka kwambiri
ndipo udani wanu pa Mulungu ndi waukulu kwambiri.
Mneneri amamuyesa chitsiru,
munthu wanzeru za kwa Mulungu ngati wamisala.
8Mneneri pamodzi ndi Mulungu wanga
ndiwo alonda a Efereimu,
koma mneneri amutchera misampha mʼnjira zake zonse,
ndipo udani ukumudikira mʼnyumba ya Mulungu wake.
9Iwo azama mu zachinyengo
monga masiku a Gibeya.
Mulungu adzakumbukira zolakwa zawo
ndipo adzawalanga chifukwa cha machimo awo.

10“Pamene ndinamupeza Israeli
zinali ngati kupeza mphesa mʼchipululu.
Nditaona makolo anu,
zinali ngati ndikuona nkhuyu zoyambirira kupsa.
Koma atafika ku Baala Peori,
anadzipereka ku fano lija lochititsa manyazi
ndipo anakhala onyansa ngati chinthu chimene anachikondacho.
11Ulemerero wa Efereimu udzawuluka ngati mbalame.
Sipadzakhalanso kubereka ana, kuyembekezera kapena kutenga pathupi.
12Ngakhale atalera ana
ndidzachititsa kuti mwana aliyense amwalire.
Tsoka kwa anthuwo
pamene Ine ndidzawafulatira!
13Ndaona Efereimu ngati Turo,
atadzalidwa pa nthaka ya chonde.
Koma Efereimu adzatsogolera
ana ake kuti akaphedwe.”

14Inu Yehova, muwapatse.
Kodi mudzawapatsa chiyani?
Apatseni mimba yomangopita padera
ndi mawere owuma.

15“Chifukwa cha zoyipa zawo zonse ku Giligala,
Ine ndinawada kumeneko.
Chifukwa cha machitidwe awo auchimo,
ndidzawapirikitsa mʼnyumba yanga.
Sindidzawakondanso;
atsogoleri awo onse ndi owukira.
16Efereimu wathedwa,
mizu yake yauma
sakubalanso zipatso.
Ngakhale atabereka ana,
Ine ndidzapha ana awo okondedwawo.”

17Mulungu wanga adzawakana
chifukwa sanamumvere Iye;
adzakhala oyendayenda pakati pa anthu a mitundu ina.
Copyright information for NyaCCL